Msonkhano waukulu wa PDP wayamba ku Blantyre
Nthumwi zayamba kufika ku Comesa Hall mu mzinda wa Blantyre komwe chipani cha People’s Development (PDP) chikuchititsa msonkhano wake waukulu.
Yemwe akugwilizira udindo wa mneneri wa chipanichi a Rhodes Msonkho wati nthumwi zokwana 1200 ndi zomwe zikuyembekezeka kufika pa malowa.
A Msonkho atinso aitana zipani zina ku msonkhanowu. Mamembala ena a chipani cha Peoples (PP) afika kale.
Mtsogoleri wa chipanichi a Kondwani Nankhumwa, omwe alibe opikisana nawo, akuyembekezeka kutsekulira msonkhanowu.
The post Msonkhano waukulu wa PDP wayamba ku Blantyre appeared first on Malawi Voice.